ABOUT

Umboni wanga ndi masamba a intaneti amene apangidwa ndi cholinga chofuna kufikila anthu ambiri mosavuta ndi maumboni ndi mauthenga a Mtumiki Twaibu Hamid Ali. Mr Twaibu Hamid Ali ndi mkhristu wa mpingo wa Seventh Day Adventist church. Chiyambi chake anapembedzapo chisilamu kenako analowa chipembedzo cha nseli cha Satana. Mr Twaibu anakhala ndi kuphunzila zambiri ndi zakuya za chipembedzo cha chisilamu chomwe anachiyamba kuyambila umwana wawo. Ali mu sichilamu Mr Twaibu anayitanidwa ndi anthu opembedza Satana kuti alowe chipembedzo chopembedza Satana malingana ndi mphamvu zakuya zamatsenga zomwe anali nazo zomwe anazipeza powelenga mabuku a zamatsenga omwe anawapeza ku chisilamu. Mr Twaibu anavomera ndipo anapembedza chipembedzo cha Satanachi kwa zaka 17. Relo Mr Twaibu atatha kutembenuka mtima nasiya zonse zonyasa zomwe ankachita kale maka-maka mu chipembedzo cha Satana, Mr Twaibu akuchenjeza anthu pa zobisika za zomwe Satana, mipingo, zipembedzo, maboma komanso anthu akhala akuchita ndi cholinga chofuna kugwetsa ufumu wa Mulungu ndi kukweza ufumu wa Satana komanso kulepheletsa anthu ambiri munjira yawo yotsatila Mulungu. 

MAUMBONI NDI MAUTHENGA

Share 

info@umboniwanga.com
+265 99204 0525

+265 88203 6003