UTHENGA WAPADELA OCHOKELA KWA MTUMIKI TWAIBU
Zikomo pobwera kumasamba athu a intaneti. Cholinga cha maumboni anga sikunyazitsa munthu, anthu, mtumiki, atumiki, mpingo, mipingo kapena gulu lina lililonse la anthu, ayi. Cholinga changa ndikungofuna kudziwitsa dziko lapansi pa zinthu zomwe ndaziona ndi kuzidziwa malingana ndi moyo umene ndakhala padziko pano. Zili ndi inu kugwilizana nazo kapena kutsutsana nazo. Zonse zomwe mutazimve mu maumboni angawa ndi zinthu zimene ndinaziona ndi kuzigwila ndipo ndikuchitila umboni kwa inu kuti ndi zoona. Pambali pa zinthu zomwe mukudziwa kale, phatikizilaninso zomwe ndikukamba mu maumboni angawa. Chisankho chikhale kwa inu kusamala za zomwe ndikunenazi kapena kungomva ndi kuzitaya. Koma ndi khumbo langa ndi cholinga changa kuti umboni wangawu ukutseguleni maso ndi kukuthandizani kayimidwe kanu mmoyo wanu padziko pano maka-makanso kayimidwe kanu mmoyo wanu wa uzimu kuti pamene Ambuye wathu Yesu Khristu akubwera, tisadzasepmphane ndi mphatso ya mtengo wa patali ya moyo wosatha. Ndikuthokozanso mwapadela kwa onse amene mukutenga gawo mukuthandizila utumikiwu kuti upite patsogolo, Mulungu akudalitseni mwapadera-dera. Amen.